Nkhondo ft. SevenOmore & GD Lyrics
- Genre:Soul
- Year of Release:2022
Lyrics
M'ma
Makadidi
Abusa mpepheleniko
Muli matenda mthupimo
Nsanje yalowa mkatimo
Abusa mpempheleniko
Ndine mfana oyimba bho
Koma ndimadana ndi anzanga oyimba kuposa ineyo
Oblowa kuposa ineyo
Chifukwa amayimba lokolo
Abusa mpempheleniko
Ndimafuna nditakhala wabwino
Koma zimangovuta mkatimo
Abusa mpempheleniko
Muli ziwanda mthupimo
Zinabwela ndi dollar zo
Abusa mpepheleniko
Ndine mfana wochita bho
Ndilinso ndi chi nkazi chabwino
Abusa mpempheleniko
Ndakosoneza banja lo
Langa ndi mzanga wabwino
Abusa mpempheleniko
Ndimafuna nditakhala wabwino
Koma zimangovuta mkatimo
Muli nkhondo muli nkhondo
Makadidido ali pa moto
Ndi chitonzo ndi chitonzo
Kukhala ochita bwino kumaloto kokha
Nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo mumtima
Ndili mumdima
Kuwala mmoyo mwanga kunazima
Kuwona ndimafuna maso anafa
Kufunitsitsa ndiye ndimafuna
Ndisiye kuzunza akazi angawa
Ndisiye kuzunza ana angawa
Ndisiye kuzunza ana amasiye
Ndisiye kubela anthu osauka
Ndimafuna nditasintha
Ndisiye kuzunguza anthu mu ghetto mwathu akumandidandaula
Ndufuna nditasintha
Ngati sukulu sindingamangile anawa ndinalowelanji m'boma
Oh my God oh my God
Abusa mundipempheleleko
Pachuluka chinyengo pa dziko
Abusa mundipempheleleko
Muli nkhondo muli nkhondo
Makadidido ali pa moto
Ndi chitonzo ndi chitonzo
Kukhala ochita bwino kumaloto kokha
Nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo
GD sewa sewa
Atate woyera Yehova wamakamu, bless
Tabwela pamaso pano ndi mwana wanu, yes
Ali ndi nkhondo mu mtima mpatseni mdalitso
Ndi ochimwa koma amafuna mparadizo
Wachimasomaso kuponya ponya diso
Ali ndi zofooka akupempha chilimbikitso
Luka 4 verse 2 yesu anayesedwa
Yang'ana Yobu chapter 1 yobu anayesedwa
Genesis 39 Yosefe anayesedwa
Chi khristu ndi nkhondo ndipo tonsefe tidzayesedwa
Satana ndi mzimu sungamuphe ndi nkondo
Nkhodo ya uzimu timamenya pa mawondo
Zimatheka kutopa Mose anakwezedwa nkono
Khala ochilimika osamangoliza nkono no no
No it's a battle for the soul
The devil creeping on a low victory is slow
We gon' win it with every blow
Imatelo nkhondo ya mu mtimamo
Muli nkhondo muli nkhondo
Makadidido ali pa moto
Ndi chitonzo ndi chitonzo
Kukhala ochita bwino kumaloto kokha
Nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo
Muli nkhondo