
Mawa Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2024
Lyrics
Lero kwacha ndi nyengo zolusa
Tsiku ladza ndi nyengo zozunza
Tili ndi mafunso opanda mayankho
Ndipo lero pali kugawikana ndi tsankho
Lero tadzuka ndi mitima yosweka
Zoti tizapeza mtendere zimaoneka
Ngati zinthu zakutulo ngati zinthu zosatheka
Chifukwa cha kulira tinaiwala kuseka
Lero tangodzadzidwa ndi mantha
Koma mawa mavuto onse adzatha
Mawa kuli chimwemwe chosalekeza
Pali tsiku lomwe misozi siidzalengeza
Ndikudziwa kukubwera tsiku
Lomwe kudzawala ukatha usiku
Ndidzapeza mayankho kumafunso anga onse
Ndidzapeza mpumulo ku mazunzo anga onse
Likubwera tsiku mawa
Sindizadanso nkhawa
Ukapita mdimawu ndikudziwa kudzacha
Ukapita mdimawu ndikudziwa kudzacha yea
Mawa mawa,mawa mawa
Mawa mawa yea
Mawa mawa, mawa mawa
Mawa mawa yea
Uwe uwe uwe uwe uwe
Mawa yea mawa yea
Uwe uwe uwe uwe
Mawa yea mawa yea
Mawa likubwera lopanda mikwingwilima
Kudzawala dzuwa ndipo udzathawa mdima
Yea tsiku lopanda zowawa
Ndipo maganizo sadzachuluka ndi nkhawa
Likubwera tsiku lopanda ululu
Tsiku la mtendere ndinso la ufulu
Tsiku lomwe mavuto alibe mpata
Kudzakhala bata ndipo mvura idzakata
Kwa ovutika mtendere ukudikilira
Komwe nkwiyo wa pa dziko pano sudzapitilira
Kwa onse olemedwa ndi amene akulira
Adzapuputa misozi ndipo adzamwetulira
Lero kuli mdima ndi mavuto
Osowetsa mtendere mpaka kumasowa tulo
Chimwemwe chidza chofufuta mavuto a dzulo
Ndipo ndikudziwa m'bandakucha udza ndi mpumulo
Likubwera tsiku mawa
Sindizadanso nkhawa
Ukapita mdimawu ndikudziwa kudzacha
Ukapita mdimawu ndikudziwa kudzacha yea
Mawa mawa,mawa mawa
Mawa mawa yea
Mawa mawa mawa mawa
Mawa mawa yea
Uh tsiku lina pa golide ndidzayenda
Mu dziko lopanda chisoni kapena matenda
Nde sindidanda ndikakhala
Ukapita mdimawu kudzabwera kuwala
Mavuto lero akamandigwera
Sangafanane ndi ulemelero ukubwera
Olo mavutowa adzitigwera
Sangafanane ndi ulemelero ukubwera