Yonah Lyrics
- Genre:Others
- Year of Release:2024
Lyrics
Mmmmmmh ooooooh ooooooh Akuzike Thawe yeahhhhhhhhh eeh eeh
Mu doko la Yoppa, Yonah anayitanidwa Kuti akalalikile ku Nineveh, ndi kuwawuza za nkwiyo WA Mulungu Koma Yonah anathawa, kupita ku gombe la kutali la Tarshish Akuyesela kuthawa, mkwiyo wa Ambuye, omwe unali kudza mtsogolo
Koma dzanja la Mulungu lili pa ife, kulikonse kumene tingapite Adzatithamangitsa, ndi chikondi chake, ndi kutibwezela kwa iye
Yonah, Yonah, mu mimba ya nsomba Chozizwitsa cha chifundo, nkhani yoti ipambane Chikondi cha Mulungu sichitha, sichidzatithawa Yonah, Yonah, mneneri, ndi uthenga woti awonetse
Nyanja yamkuntho, inkachita chipwilikiti Asilikali anapemphela, kwa milungu yawo, koma yonah ankadziwa zomwe akuwona Anawauza za kusamvela kwake, ndi Mulungu amene anasiya Anamponya m'nyanja, ndipo nyanja inayamba kudekha
Koma dzanja la Mulungu lili pa ife, kulikonse kumene tingapite Adzatithamangitsa, ndi chikondi chake, ndi kutibwezela kwa iye
Yonah, Yonah, mu mimba ya nsomba Chozizwitsa cha chifundo, nkhani yoti ipambane Chikondi cha Mulungu sichitha, sichidzatithawa Yonah, Yonah, mneneri, ndi uthenga woti awonetse
Masiku atatu ndi usiku, m'kati mwa nsomba Yonah anapemphela, ndi kulapa, ndipo Mulungu anamva kulila kwake Nsomba inamulavula pa gombe la mchenga Ndipo yonah anapita, ku Nineveh, kulalikila, ndi kukonda
Anthu a ku Nineveh, anamvela kuitana kwake Analapa, ndi kutembenukila, ku mtima wachikondi wa Mulungu, pambuyo pake Njila zawo zoipa, zinakhululukidwa, ndipo anapulumutsidwa Chozizwitsa cha chifundo, chomwe sichingafanane