Fanizo La Tiligu Lyrics
- Genre:Others
- Year of Release:2024
Lyrics
Mmmmmmh ooooooh ooooooh Akuzike Thawe yeahhhhhhhhh eeh eeh
Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake; koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tiligu, nachokapo
Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole
Kazilekeni zonse ziwili, zikulile pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tiligu m'nkhokwe yanga
Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokela kuti namsongoleyo?
Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole
Kazilekeni zonse ziwili, zikulile pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tiligu m'nkhokwe yanga
Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye