Ukwati Wa Ku Kana Lyrics
- Genre:Others
- Year of Release:2024
Lyrics
Mmmmmmh ooooooh ooooooh Akuzike Thawe yeahhhhhhhhh eeh eeh
Pa tsiku lachitatu panali ukwati ku Kana wa ku Galileya
Amayi a Yesu anali komweko, ndipo Yesu ndi ophunzila ake anaitanidwa Vinyo atatha, a make a Yesu ananena kwa Iye "Alibe vinyo"
Nthawi inali itakwana, kuti Yesu awulule
Ulemelelo wake ndi mphamvu zake, m'njira yodabwitsa kumva Vinyo anatha, koma Yesu anali atangoyamba kumene Kuti awonetse ulemelelo Wake, kwa aliyense
Aleluya, Yesu ndiye amene asandutsa madzi kukhala vinyo
Aleluya, Iye ndi Mfumu ya mafumu, amene ali wamphamvu ndi Waumulungu
Aleluya, ulemerero Wake wawululidwa, mu chizindikilo chozizwitsa ichi
Yesu anati kwa iye, Mkazi, ichi chiri chotani ndi Ine?
Nthawi yanga sinafike"
Amake adanena kwa atumiki, Chitani chilichonse chimene angakuuzeni.
Kumeneko kunali mitsuko yamadzi isanu ndi umodzi yochitira mwambo wachiyeretso wa Ayuda
Nthawi inali itakwana, kuti Yesu awulule
Ulemelelo wake ndi mphamvu zake, m'njila yodabwitsa kumva
Vinyo anatha, koma Yesu anali atangoyamba kumene
Kuti awonetse ulemerero Wake, kwa aliyense
Aleluya, Yesu ndiye amene asandutsa madzi kukhala vinyo
Aleluya, Iye ndi Mfumu ya mafumu, amene ali wamphamvu ndi Wa umulungu
Aleluya, ulemelelo Wake wawululidwa, mu chizindikilo chozizwitsa ichi
Yesu anati kwa antchito, Dzazani mitsukoyo ndi madzi.
Ndipo adazidzaza mpaka pamlomo
Ndipo anati kwa iwo, Tulani tsopano, mupite nayo kwa mkulu wa phwando.
Chotero anamtengera kwa iye, ndipo iye analawa madzi amene anasanduka vinyo
Nthawi inali itakwana, kuti Yesu awulule
Ulemelelo wake ndi mphamvu zake, m'njira yodabwitsa kumva
Vinyo anatha, koma Yesu anali atangoyamba kumene
Kuti awonetse ulemelelo Wake, kwa aliyense
Aleluya, Yesu ndiye amene asandutsa madzi kukhala vinyo
Aleluya, Iye ndi Mfumu ya mafumu, amene ali wamphamvu ndi Waumulungu
Aleluya, ulemelelo Wake wawululidwa, mu chizindikilo chozizwitsa ichi
Mkulu wa phwando adayitana mkwatiyo nanena naye "Munthu aliyense ayambe apereka vinyo wokoma, ndipo anthu akaledzera, kenako amapereka vinyo wosauka Koma iwe wasunga vinyo wabwino kufikira tsopano lino"
Mmmmmmh ooooooh ooooooh Akuzike Thawe yeahhhhhhhhh eeh eeh