Ghetto ft. ProVoice Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2024
Lyrics
Komwe ndakulira ndiku ghetto kwa Biwi
Kunandipanga kukhala katswiri
Ima ndikuuze mbiri
Moyo umachoka kutali
Tinali mafana osadandaula
Pano aliyense akukula
Ma pressure kufuna kupeza mula
Ena anaiphula
Kuiwala komwe tachokela
Kuba money yaku maliro
Kudzipatsa tokha malipilo
Kusokoneza kusukulu
Kukana nyemba adzukulu
Kulowa ma crew 2 finger ku culture
Tinali abwino kukacha
Ma baby kupanga uhule
Money yachidule
Zambiri ine sindingaulule
Ndakulira mu ghetto
Zambiri ndaphunzira
M'mene moyo ukhalira
Singaiwale ghetto
Malo omwe takulira
Anthu omvana a nsangala
Ma Baby ali mu Ghetto
Ma Shasha ali mu Ghetto
Kunjoya kuli mu Ghetto
Zikhomo zili mu Ghetto
Kobadwila sungatchuze ndikuuze
Kothela ndikomwe ungakonze
Ku ghetto kwachoka ma superstar
They came a long way too far
Ambiriwa anachokela mu ghetto
Ma CEO achokela mu ghetto
Ma president achokela ghetto
Bwanji ukuziphweketsa chifukwa ndiwa ghetto?
Osakhala waulesi
Ipatse moto machesi
Palibe choletsa success
Iweso utha kusintha mu mchesi
Olo a Mpinganjira
Anakumana nzopinga mu njira
Kuphushabe nkuiphula
Iweso phusha osangokhala
Ndakulira mu ghetto
zambiri ndaphunzira
M'mene moyo ukhalira
Singaiwale ghetto
Malo omwe takulira
Anthu omvana a nsangala
Ma Baby ali mu Ghetto
Ma Shasha ali mu Ghetto
Kunjoya kuli mu Ghetto
Zikhomo zili mu Ghetto