Ntchito Lyrics
- Genre:Gospel
- Year of Release:2023
Lyrics
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Ankasakasaka daily mmm mmm
Anayipeza ntchito
Ey Ey
Panali nkulu wina wake
Dzina lake Timoteyo
Anali mnyamata wolimbika
Moti anthu ambiri amatero
Ankakhonza ali ku skulu
Anamusankhira ku ya Ukachenjede
Koma chomwe sanamuwuze
N'choti ukamaliza skulu ukachenjere
Ankangodziwa ngati ufuna kukhala bwana
Ulimbikire skulu udakali mwana
Anayesetsa ndithu nkupita college
Mpaka kumaliza ntchito sanamukhole eti
Ankawona ngati kuti n'chabe nthawi
Idzakwana yokha sadzakhala mphawi
Koma chaka mpaka chaka nkumadutsa
Osapeza ntchito iye nkumafunsa
Kodi ndinalakwa chani?
Ndikhala lova moyo wanga wonse man?
Komabe sanachite mphwayi
Anaponyaponya ma CV nde mwa mwayi
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Ankasakasaka daily mmm mmm
Anayipeza ntchito
Anasangalala atayipeza
Sankhakhulupilira kuti zatheka
Anayamika Mulungu nkumukweza
Kukumbukira komwe akuchokera
Zaka zinayi ali opanda ntchito
Nkumawona ngati ndi opanda ntchito
Analonjeza kuti akazayiphula
Azayisamala sazayibudhula
Komano nthawi nkumapita
Anayamba kuyiwala ankayamika
Abwana akamupatsira chokachita
Amatero komatu monyinyirika
Akatere Timoteyo nkumasinkha
Ntchito yomweyi mpaka ine nzifinyika
Ankawona ngati wafika
Anasiya kulimbikira akafika
M'mamawa amakhalira bhawa
Masana samkhala amathawa
Akampatsira Ntchito iye amakana
Amvekere kuti ndiyipanga mawa
Mawa lakelo litafika
Anamupatsira kalata azipita
Yeah
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Analembedwa ntchito mmmmmmm mmm mmm
Ankasakasaka daily mmm mmm
Anayipeza ntchito
Ayeyiyeyiyeaaah eh
Ayeyiyeyiyeaah
Ayeyiyeyiyeaaah eh
Ayeyiyeyiyeaah
Ayeyiyeyiyeaaah eh
Ayeyiyeyiyeaah
Ayeyiyeyiyeaaah eh
Ayeyiyeyiyeaah
Anthu ambiri tikakhala mu utchimo
Timakhala kuti tili pa chiphinjo
Sitidziwa kuti tingasiye bwanji
Timasowa mtendere muntima nanji
Nde Mulungu akatipulumutsa
Chisomo chke chimakhala chatikhudza
Timayenera kuti timuyamike
Tisayiwale popanda iye tinalibe
Chikhulupiliro chathu ndi chisomo
Timayenera kuti tigwire ntchito
Osabwelera ku utchimo
Tizidzilora kuti tife ku dziko
Palibe ntchito yopanda bwana
Kuti uyisunge osapanga zibwana
Panga zomwe bwana wako wakutuma
Osakomedwa ndi nthawi yongopuma
Nde ena tili ndi ntchito
Yosamala banja lathunso ndi ntchito
Osangokonda ntchito yokha nkuyiwala
Kuti tinkafuna banja nafe tili single
Ambiri tili pa chi ntchito
Osafowoka tiyeni tilimbike
Ngati usakugwilira ntchito Yesu
Ukugwilira ntchito winayo udziwe
(Think about it)
Yeah
Tinalembedwa ntchito (Palibe anatikakamizatu ndi tokha)
Tinalembedwa ntchito (Tinka guba tinka guba tinkagubilayeee)
Tinalembedwa ntchito (Palibe anatikakamizatu ndi tokha eh)
Tinkasakasaka daily (Yey yey yehh)
Tinayipeza ntchito (Owoowoooh)
Ayeyiyeyiyeaaah eh
Ayeyiyeyiyeaah
Ayeyiyeyiyeaaah eh
Ayeyiyeyiyeaah
Ayeyiyeyiyeaaah eh (Tinka guba tinka guba tinkagubilayeee)
Ayeyiyeyiyeaah
Ayeyiyeyiyeaaah eh (Woowooowooh)
Ayeyiyeyiyeaah