Alipo Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2022
Lyrics
Alipo - EvanzMuzik
...
Ndilindi×2 nkhani inayake itha kukusinthani
Mawumboni ati idachitika ku sudan
Ati kunali nkhondo yolimbilana migodi
Malebo ndimifuti yawo shooting everybod
Anthu amathawa kukasaka m'mtendele
Tsoka kwankhalamba ndiana achichepele
M'mene ndinavela ati zidayenda chonchi
Mabanja atatu adathawila limodzi
Ulendo wawo unali odutsa nchipululu
Njoka, njala ndi ludzu kuwavetsa ululu
Atayenda mitunda then adapeza deni
Yomangidwa maluso galu alipa tcheni
Atayesa kugogoda palibe amayakha
Adangokhala pakhonde kungosowa chopanga
M'dima unagwa mwini nyumba sadafike
Anaganiza zongolowa chichitike chichitike
Nde one week kutha mpaka mwezi kutha
Ndithu mpaka chaka mwini nyumba sali nkudza
Adamanga maziko nyumba zina adadzutsa
Adayamba kuchulukana ngati siwodutsa
Muntima amadziwa kuti nyumbayo siyawo
Iwo ndongopitilila pawulendo wawo
Ndipo tsiku linalake mwini wake akadzabwela
Adzafusa mafuso oti kuyakha adzalephela
Ndimene timakhalila padziko
Timakhala busy ndikumanga maziko
Zinthu zozipeza mpaka nsanje ndi kupha
Zose ndizotsala kumanda kulibe thumba
Mwina ndinu achuma mayendapo m'mayiko
Kapena ndinu ophunzila ndithu pomwe mulipo
Zosezi mukamaziona musazitenge simple
Mwiniwake wadzikoli alipo×4