
Muwasunge Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2025
Lyrics
Mu mtima muli nkhawa ndi zinkhani
Akukhala moyo osiyana ndi chomwe anali
Zambiri zinalakwika pachiyambi
Ali nfana sanasamale za tsogolo ndi nthawi
Ankapusitsika ndi za pa social media
Kupanga impress anthu oti sankamudziwa
Ikakhala geli ati sankaifila
M'dala inkapheya fees inangotopa ndikusiya
Pano amazimvera chisoni
Akakumbukira zimangothera misonzi
Ma best friend onse aja ali ndi zi ma plot
Anasiyana zochita sangachezenso limodzi
It was party after party
Atchene aoneke bho amufile ma guy
Akudikilira mwezi uthe kaye
Ikangolowa salary ya blesser avaye pena pake
She was just a little girl
Nthawi imeneyo ali ndi zaka 16
Tinkangomva kambiri nfanayu ndi sley queen
Panopa anangotsala ndi zithunzi za ku HD
She is now turning 25
And she really wanna settle down
She really wants a better man
Azamusamale pamodzi ndi ana ake
Zotsatira za tchimo kuwawa
Aliyense amakolola zomwe amadzala
Koma poti ndife anthu pena timaiwala
Tikamapanga zisankho sitiganiza za mawa
Achinyamata tachulutsa masewera
Chifukwa cha ushasha tikutailira pena
Zolakwa zathu zomwe timablema nazo ena
Koma mapeto ake timakhala olephera
Akamatidzudzula ife timanyozera
Ndikumasowa potsamila mavuto akatigwera
Ma regret pa zinthu zoti tikanatha kupewa
Taononga tsogolo chifukwa cha kusamvera
Vuto lathu lili mumtima
Mwangodzadza zinthu zosafunikira
Koma tikulephera kuzindikira
Ndichifukwa zikumatikanika kusintha
Aliyense ndi munthu amalakwitsa
Koma ndi udindo wathu obweretsa kusintha
Aliyense ndi munthu amalakwitsa
Koma ndi udindo wathu obweretsa kusintha
Ambuye muwasunge ana anga
Muwateteze kuzotsatira za machimo anga
Asazakhale ma victim azolakwa zanga
Musazawalange chifukwa cha kusamva kwanga
I wanna be a responsible father
Ndizakhale role model wa mafana anga
Komanso lizizaopa Mulungu banja langa
Kupemphera nthawi zonse ka family kozitsata
Mundithandize kukonza njira yanga
Ndikudziwa tsogolo langa lili m'manja mwanga
Lili mu zisankho zanga lili mu zochita zanga
Kuganiza kwanga nkomwe kungasinthe moyo wanga
Chonde anawo muwasunge
Pomwe ndinalakwa ngati kholo mukhululuke
Mbewu zoipa zomwe ndinazidzala muzizule
Tambasulani nkono wanu Ambuye muwakhudze
Imvani pemphero langa
Muzawapatse nzeru ana anga
Imvani pemphero langa
Ana anga azakhalenso chimwemwe changa
Anawo muwasunge
Anawo muwasunge