
Mtima_Wanga Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2025
Lyrics
Life is unpredictable
Chonde mtima wanga uzidekha
Kumasamala popanga zisankho
Tsogolo lako si udindo wa anthu ena
Osamapusitsika ndi za pa social media
Kuseli kwa ma post ambiriwa akuvutika
Kumapempha nzeru zinthu zikakukulira
Size ilibe ntchito nyengo zikafuna kusintha
Zomwe umafuna pena si zomwe umazipeza
Koma osamazipatsa unnecessary pressure
Anthu samasamala za momwe umamvera
Akamakunyoza chonde osamawatengera
Uzidekha mtima wanga uzidekha
Usaiwale chomwe uli chifukwa cha anthu ena
Uzipemphera mtima wanga uzipemphera
Mtendere sumasowa kwa omudziwa Namalenga
Put your past behind your back and focus on your future
Yesu ndiye njira iwe ndi ine ongodutsa
Munthu akakulakwira kumakhululuka
Yes you can be perfect by just being who you are
Okondedwa mtima wanga
Tchera khutu imva kulankhula kwanga
Uzisiyanitsa abale ndi anzanga
Tonse ndi anthu koma kuganizaku nkosiyana
Kumayamika ukapeza okukonda
Poti zoterezi masiku ano zimasowa
Usamadele nkhawa ndi omwe amakulonda
Pa mavuto pa mtendere nthawi zonse uzikondwa
Udziwe za kufunikira kwako
Ataye awo ngati alibe nawe ntchito
Usakhale kapolo wa thandizo lawo
Dziwa chilichonse chomwe uli nacho ndi m'dalitso
Usamafile bitter ndi kupambana kwa wina
Chiyambi chako ndi zotsatira zawo uzisiyanitsa
Mavuto amabwera ndikupita
Uzingoika chidwi pa zinthu zopindulitsa
Uziopa Mulungu mtima wanga
Ndizomwe zingandipangitse kusiyana ndi anzanga
Nzeru zochokera kumwamba
Ndizomwe zingabweretse kusintha pa moyo wanga
Chinanso kumakhala ozichepetsa
Koma osamazionera pansi wekha
Ulendo wakuchita bwino ulibe pothera
Chonde osaluza hope chifukwa chakulephera
Ndikagwa uzinditola
Uzinditeteza kuzomwe sindingathe kuziona
Pano dzikoli linaopsa
Moyo ndi ulendo koma osamangotengeka ngati matola
Always be courageous atero malemba
Osamatopa ndikumazikhulupilira wekha
Maganizo ako ndi yankho la mavuto onsewa
Ndi chisomo cha Mulungu chilichonse ndichotheka