
Olakwa Ndani? Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2024
This song is not currently available in your region.
Lyrics
Olakwa Ndani? - Macelba
...
Olakwa ndani olakwa ndani
pakati pa ochotsa mimba kapena oikana
Okana kholo kapena okana mwana
pakati pa hule loima cha pa stereo
kapena sisitele amene akuyenda ndi ansembeyo
olakwa ndani?
Dona yoti yavutika ndalama ya fees
kuti ayipeze basi agone ndimabiggie
Kapena dolo woti moyo wake sizikuyenda
Kamba koopa moyo wakuba kutenga chingwe nkuzikhweza aah
olakwa ndani?
ovotera munthu chifukwa anahongedwa
Kapena awa awa osavota nkomwewa
Zikavuta pamawa kulodzana dzala
olakwa sine koma ndiwe koma olakwa
olakwa ndani ? (ooh ndiuze) olakwa ndani ? (ooh ndiuze) koma olakwa ndani? (ooh ndiuze) olakwa ndani? olakwa ndani
Olakwa ndani munathawa dala geli nokha adona
Moyo wanu opanda mapepalawo
Mwapita Ku interview ndipo bwana wanenetsa
Carpet interview kuti akulembeni ntchito
olakwa ndani
Nokha mwatenga chuma nkupatsa a prophet
Nkhosa zikumanana nkumadyetsa a prophet
Nokha mwayambaso kumanyoza ma prophet
Chuma mudzikundikila Malo motitumikira
Ndani?
Ogwetsa kwacha kapena obisa kwacha
Ochulukitsa nsokho kapena othawa nsokho
Lero zavuta tayamba kulodzana dzala
Olakwa sine koma iwe
koma olakwa
Olakwa ndani? (ooh ndiuze) olakwa ndani? (ooh ndiuze) olakwa ndani (ooh ndiuze) olakwa ndani (oooh ndiuze) olakwa ndani
Lyrics written by Blessings Mphongolo Sàínt..