PULANI YA YEHOVA Lyrics
- Genre:Others
- Year of Release:2024
Lyrics
Pulani ya yehova palibe angatsutsane nayo
Pulani ya yehova palibe angatsutsane nayo
Palibe palibe palibe nso
Palibe angatsutsane nayo
Ndamva zoti mudakambilana mundigulitse
Kufuna funa pulani yoti ndithe
Moyo wanga ukamayenda sim'mamva bwino
ah ah ndidakulakwirani chani kodi?
Nde paja amati mtengo obala zipatso
umagendedwa theladi ndi izi
kukhala nanu bwino bwino kuyendera limodzi
Koma mukusunga lupanga ku mphasa
Koma choti mudziwe chomwe Yehova
Adaika mwa Ine, palibe angachichotse
Pulani ya yehova palibe angatsutsane nayo
Pulani ya yehova palibe angatsutsane nayo
Palibe palibe palibe nso
Palibe angatsutsane nayo
Adayesa kumpondereza mwana Davite
Ali aka nkhondo sikangamenye
Ankaona m'sinkhu mwa Iye mwa iye osati Yehova
Mpaka nkhondo mwanayi adapambana
Olo dziko liyike malire ngati Yehova walemba akwanilitsa
Pulani ya yehova palibe angatsutsane nayo
Pulani ya yehova palibe angatsutsane nayo
Palibe palibe palibe nso
Palibe angatsutsane nayo
Palibe palibe palibe nso
Palibe angatsutsane nayo
Palibe palibe nso
Palibe palibe nso yeh
Onga Inu Baba
Palibe palibe nso
Bwana wa ma bwana
Palibe palibe nso