Kuthokoza ft. Tadala Lyrics
- Genre:Hip Hop & Rap
- Year of Release:2023
Lyrics
Kunja kwacha, dzuwa latuluka. Anthu alowe komwe amasaka ndalama, eeh, koma tisananyamuke kumathokoza Mulungu mu zonse eeeh
Kuyamika mu zonse ngakhale zonse ndi chabe
Zisachite kufika poti mpakana ndikabe
Zochepazi ziphukile
Mtima wanga ukhutile
Ngati chinga gile nkabwelela mundichingamile
Zinsinsi za moyo mundiululire
Zipatso za moyo mundipululire
Moto wanyanya nkhuni mutifumilile
Dziko kuzungulira osadabwa zizungulire
Sinkumila ndikuyandama
Osaodzela ndikuyang'ana
Zisomo zake zingotsagana
Ndinali yani dzana
Lero ndine nyali dzana timangonamizana
Sinditama munthu kuwopa mwina andimana
Mu m'bwaa zanga ukhwepa
Panga zaine mpakana mtembo useka
Kumbwambwana ambwana
Kumazinyenga kupambana
Zako nzake zake namana kumkhwapa napana
Lero ndingothokoza
Mu zonse inu nditsogoza
Kusekelela otonza
Sazagwetsedwa otonza