
Namondwe Lyrics
- Genre:Others
- Year of Release:2024
Lyrics
Kunena zoona ndatopa
I don't think I have it in me anymore
Kuyesa nde ndayesa nkuthodwa
Koma sizikuyenda konse
Ndimvelenikoni ndavuka
Kuphusha ndikuphusha koma sizikusuntha
Kumafuna kulila
Misonzi sikutuluka
Ambuye ngati mukundinva
Ilamuleni nyanja kuti ichite bata
Ngalawa yanga ikumila sinditha kusambila
Musalole
Kuti namondwe anditenge
Namondwe anditenge anditenge
Musalole
Kuti namondwe anditenge
Namondwe anditenge
Anditenge
Musalole
Nyali yanga izime
Ndikamagwa mundigwile
Ndisamazikaikile ndisazilembele malire
Kuthekela ndilinako kokwanilisa
Ndikayamba filimu nzimalizisa
Chilichonse mmalo mwake mwaikiza
Ngati si changa ndizitha kuziwa
Sinzikakamiza
Musalole
Kuti namondwe anditenge
Namondwe anditenge anditenge
Musalole
Kuti namondwe anditenge
Namondwe anditenge
Anditenge
Musalole